Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 12:6-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo mfumu Rehabiamu anafunsira kwa mandoda, amene anaimirira pamaso pa Solomo atate wace, akali moyoiyeyo, nati, Inu mundipangire bwanji kuti ndiyankhe anthu awa?

7. Ndipo iwo anamuuza kuti, Mukakhala inu mtumiki wa anthu awa lero, ndi kuwatumikira ndi kuwayankha ndi kukamba nao mau okoma, tsono iwo adzakhala cikhalire atumiki anu.

8. Koma iye analeka uphungu wa mandodawo, umene anampangirawo, nakafunsira kwa acinyamata anzace oimirira pamaso pace,

9. nati kwa lwo, Kodi inu mundipangire bwanji kuti tiyankhe anthu awa anandiuza ine, kuti, Mupepuze gori limene atate wanu anatisenza ife?

10. Ndipo acinyamata anzace ananena naye, Dati, Mzitero ndi anthu awa adalankhula nanu, nati, Atate wanu analemeretsa gori lathu, koma inu mutipepuzire limenelo; mzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'cuuno mwa atate wanga.

11. Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzani gori lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa gori lanu, atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.

12. Ndipo Yerobiamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehabiamu tsiku lacitatu monga momwe anawauzira mfumu, nati, Bweraninso kwa ine tsiku lacitatu.

13. Ndipo mfumu inayankha anthu mau okalipa, naleka uphungu anampangira mandodawo,

14. nalankhula nao monga mwa uphungu wa acinyamata, nati, Atate wanga analemeretsa gori lanu, koma ine ndidzaonjezerapo pa gori lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira,

15. Potero mfumu siinamvera anthuwo, pakuti kusintha uku kunacokera kwa Yehova, kuti akhazikitse mau ace amene Yehova ananenetsa Abiya wa ku Silo kwa Yerobiamu mwana wa Nebati.

16. Ndipo pakuona Aisrayeli onse kuti mfumu siinawamvera iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tiri naye ciani Davide? inde tiribe colowa m'mwana wa Jese; tiyeni kwathu Aisrayeli inu; yang'aniranitu, nyumba yako, Davide. Momwemo Aisrayeli anacoka kumka ku mahema ao.

17. Kama ana aja a Israyeli akukhala m'midzi ya Yuda, Rehabiamu anakhalabe mfumu yao.

18. Pamenepo mfumu Rehabiamu anatuma Adoramu wamsonkho, ndipo Aisrayeli onse anamponya miyala, nafa. Ndipo mfumu Rehabiamu anafulumira kulowa m'gareta wace kuthawira ku Yerusalemu.

19. Motero Aisrayeli anapandukana ndi nyumba ya Davide kufikira lero.

20. Ndipo kunali, atamva Aisrayeli onse kuti Yerobiamu wabweranso, anatuma kumuitanira iye kumsonkhano, namlonga iye mfumu ya Aisrayeli onse; palibe munthu anatsata nyumba ya Davide koma pfuko lokha la Yuda.

21. Ndipo Rehabiamu anafika ku Yerusalemu, nasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda, ndi pfuko la Benjamini, ankhondo osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, kuyambana nayo nyumba ya Israyeli, kubwezanso ufumu kwa Rehabiamu mwana wa Solomo.

22. Ndipo mau a Mulungu anafika kwa Semaya mneneri wa Mulungu, nati,

23. Lankhula kwa Rehabiamu mwana wa Solomo mfumu ya Yuda, ndi kwa nyumba yonse ya Yuda, ndi Benjamini, ndi kwa anthu otsalawo, nuti,

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 12