Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 12:19-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Motero Aisrayeli anapandukana ndi nyumba ya Davide kufikira lero.

20. Ndipo kunali, atamva Aisrayeli onse kuti Yerobiamu wabweranso, anatuma kumuitanira iye kumsonkhano, namlonga iye mfumu ya Aisrayeli onse; palibe munthu anatsata nyumba ya Davide koma pfuko lokha la Yuda.

21. Ndipo Rehabiamu anafika ku Yerusalemu, nasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda, ndi pfuko la Benjamini, ankhondo osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, kuyambana nayo nyumba ya Israyeli, kubwezanso ufumu kwa Rehabiamu mwana wa Solomo.

22. Ndipo mau a Mulungu anafika kwa Semaya mneneri wa Mulungu, nati,

23. Lankhula kwa Rehabiamu mwana wa Solomo mfumu ya Yuda, ndi kwa nyumba yonse ya Yuda, ndi Benjamini, ndi kwa anthu otsalawo, nuti,

24. Yehova atero, Musamuka, ndipo musakayambana ndi abale anu ana a Israyeli, bwererani yense kunyumba kwace; popeza cinthuci cacokera kwa Ine. Ndipo iwo anamvera mau a Yehova, natembenuka, nabwerera monga mwa mau a Yehova.

25. Ndipo Yerobiamu anamanga Sekemu m'mapiri a Efraimu, nakhalamo, naturukamo, namanga Penueli.

26. Ndipo Yerobiamu ananena m'mtima mwace, Ufumuwu udzabwereranso ku nyumba ya Davide.

27. Anthu awa akamakwera kukapereka nsembe m'nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, pamenepo mitima ya anthu awa idzatembenukiranso kwa mbuye wao, kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda; ndipo adzandipha, nadzabweranso kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda.

28. Potero mfumu inakhala upo, napanga ana a ng'ombe awiri agolidi, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisrayeli inu milungu yanu imene inakuturutsani m'dziko la Aigupto.

29. Ndipo anaimika mmodzi ku Beteli, naimika wina ku Dani.

30. Koma cinthu ici cinasanduka: chimo, ndipo anthu anamka ku mmodziyo wa ku Dani.

31. Iye namanga nyumba za m'misanje, nalonga anthu acabe akhale ansembe, osati ana a Levi ai.

32. Ndipo Yerobiamu anaika madyerero mwezi wacisanu ndi citatu, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi olingana ndi madyerero aja a ku Yuda, napereka nsembe pa guwa la nsembe; anatero m'Beteli, nawaphera nsembe ana a ng'ombe aja anawapanga, naika m'Beteli ansembe a misanje imene anaimanga.

33. Ndipo anapereka nsembe pa guwa la nsembe analimanga m'Beteli, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi wacisanu ndi citatu, m'mwezi umene anaulingirira m'mtima mwa iye yekha, nawaikira ana a Israyeli madyerero, napereka nsembe pa guwa la nsembe, nafukiza zonunkhira.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 12