Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 11:26-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo Yerobiamu mwana wa Nebati M-efrati wa ku Zereda mnyamata wa Solomo, dzina la amace ndiye Zeruwa, mkazi wamasiye, iyenso anakweza dzanja lace pa mfumu.

27. Ndipo cifukwa cakukweza iye dzanja lace pa mfumu ndi cimeneci: Solomo anamanga Milo, namanganso pogumuka pa linga la mudzi wa Davide atate wace.

28. Ndipo munthu ameneyo Yerobiamu anali ngwazi; ndipo pamene Solomo anamuona mnyamatayo kuti ngwacangu, anamuika akhale woyang'anira wa nchito yonse ya nyumba ya Yosefe.

29. Ndipo kunali nthawi yomweyo kuti Yerobiamu anaturuka m'Yerusalemu, ndipo mneneri Ahiya wa ku Silo anampeza m'njira; tsono iyeyo anabvaliratu cobvala catsopano, ndipo iwo awiri anali okha kuthengo.

30. Ndipo Ahiyayo anagwira cobvala cace catsopano, nacing'amba khumi ndi pawiri.

31. Nati kwa Yerobiamu, Takwaya magawo khumi; popeza atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Taona ndidzaung'amba ufumu m'dzanja la Solomo ndi kukupatsa iwe mafuko khumi.

32. Koma iye adzakhala nalo pfuko limodzi, cifukwa ca Davide mtumiki wanga, ndi ca Yerusalemu, mudzi umene ndinausankha m'mafuko onse a Israyeli.

33. Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitoreti mulungu wa Azidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amoabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kucita cimene ciyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wace.

34. Koma sindidzalanda ufumu wonse m'dzanja lace, koma ndidzamkhalitsa mfumu masiku ace onse, cifukwa ca Davide mtumiki wanga amene uja ndinamsankha, cifukwa kuti anasunga malamulo anga ndi malemba anga.

35. Koma ndidzalanda ufumu m'dzanja la mwana wace, ndi kupatsa iwe mafuko khumi amene.

36. Ndipo ndidzamninkha mwana wace pfuko limodzi, kuti Davide mtumiki wanga akhale cikhalire ndi nyali pamaso panga m'Yerusalemu, mudzi umene ndinadzisankhira kuikapo dzina langa.

37. Ndipo ndidzakutenga iwe, ndipo udzacita ufumu monga umo ukhumbira moyo wako, nudzakhala mfumu ya Israyeli.

38. Ndipo kudzakhala kuti ukadzamvera iwe zonse ndikulamulirazo, nukadzayenda m'njira zanga ndi kucita cilungamo pamaso panga, kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga anatero Davide mtumiki wanga pamenepo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndidzakumangira ndi kukukhazikitsira nyumba, monga nelinammangira Davide, ndipo ndidzakupatsa iwe Israyeli.

39. Ndipo cifukwa ca ici nelidzazunza mbumba ya Davide, koma si masiku onse ai.

40. Cifukwa cace Solomo anafuna kupha Yerobiamu, ndipo Yerobiamu anathawira ku Aigupto kwa Sisaki mfumu ya Aigupto, nakhala m'Aigupto kufikira imfa ya Solomo.

41. Ndipo macitidwe otsiriza a Solomo, ndi nchito zace zonse anazicita, ndi nzeru zace, kodi sizilembedwa zimenezo m'buku la madtidwe a Solomo?

42. Ndipo masiku amene Solomo anakhala mfumu ya Aisrayeli onse m'Yerusalemu anali zaka makumi anai.

43. Ndipo Solomo anagona ndi makolo ace, naikidwa m'mudzi wa Davide atate wace; ndipo Rehabiamu mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 11