Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 10:17-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndi malihawo mazana atatu a golidi wonsansantha, libawo limodzi linapangidwa ndi miyeso itatu ya golidi; ndipo mfumu inazisungira zonse m'nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano.

18. Ndipo mfumu inapanga mpando waukulu wacifumu waminyanga, naukuta ndi golidi woyengetsa.

19. Mpandowo wacifumu unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndi pamwamba pa mpando wacifumu panali pozungulira kumbuyoko, ndipo munali ngati manja m'mbali zonse ziwiri za pokhalirapo, naimika mikango iwiri m'mbali mwa manjawo.

20. Ndipo anaimikamikango khumi ndi iwiri mbali yina ndi yina, pa makwerero asanu ndi limodzi aja; m'dziko liri lonse tina simunapangidwa wotere.

21. Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomo zinali zagolidi, ndi zotengera zonse za nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano zinali zagolidi yekha yekha, panalibe zasiliva, pakuti siliva ana ngoyesedwa opanda pace masiku onse a Solomo.

22. Popeza mfumu inali nazo panyanja zombo za ku Tarisi, pamodzi ndi zombo za Hiramu; zombo za ku Tarisi zinafika, kamodzi zitapita zaka zitatu, ziri nazo golidi, ndi siliva, ndi minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za maanga maanga.

23. Ndipo mfumu Solomo anawaposa mafumu onse a dziko lapansi pa cuma ndi nzeru.

24. Ndipo anthu onse a pa dziko anafuna nkhope ya Solomo, kudzamva nzeru zace zimene Mulungu analonga m'mtima mwace.

25. Ndipo akafika munthu yense ndi mtulo wace, zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolidi, ndi zobvala, ndi zida, ndi zonunkhira, ndi akavalo, ndi nyuru; momwemo caka ndi caka.

26. Ndipo Solomo anasonkhanitsa, magareta ndi apakavalo; anali nao magareta cikwi cimodzi mphambu, mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi mphambu ziwiri, nawasungira m'midzi yosungamo magareta, ndi kwamfumu m'Yerusalemu.

27. Ndipo mfumu inacurukitsa siliva ngati miyala m'Yerusalemu, ndi mitengo yamikungudza anailinganiza ndi mikuyu ya m'madambo.

28. Ndipo akavalo a Solomo anacokera ku Aigupto; anthu a malonda a mfumu anawagula magulu magulu, gulu liri lonse mtengo wace.

29. Ndipo gareta limodzi linacokera kuturuka m'Aigupto mtengo wace masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wace masekeli zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemonso iwo anawagulira mafumu onse a Ahiti ndi mafumu a Aramu.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 10