1. Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati,
2. Kulamulira ndi kuopsa kuti ndi Iye;Acita mtendere pa zam'mwamba zace.
3. Ngati awerengedwa makamu ace?Ndipo ndaniyo, kuunika kwace sikumturukira?
4. Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu?Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?
5. Taonani, ngakhale mwezi ulibe kuwala;Ndi nyenyezi siziyera pamaso pace;
6. Kopambana kotani nanga munthu, ndiye mphutsi!Ndi wobadwa ndi munthu, ndiyo nyongolotsi!