Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 5:25-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo pomwepo anaimirira pamaso pao, nasenza cimene adagonapo, nacokapo, kunka kunyumba kwace, wakulemekeza Mulungu.

26. Ndipo cizizwo cinagwira anthu onse, ndipo analemekeza Mulungu nadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Lero taona zodabwitsa.

27. Ndipo zitatha izi iye anaturuka, Danna munthu wamsonkho, dzina lace Levi, alikukhala polandira msonkho, nati kwa iye, Unditsate Ine.

28. Ndipo iye anasiya zonse, nanyamuka, namtsata iye.

29. Ndipo Levi anamkonzera iye phwando lalikuru kunyumba kwace; ndipo panali khamu lalikuru la amisonkho, ndi enanso amene analikuseama pacakudya pamodzi nao.

30. Ndipo Afarisi ndi alembi ao anang'ung'udza kwa ophunzira ace nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ocimwa?

31. Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Amene ali olimba safuna sing'anga; koma akudwala ndiwo.

32. Sindinadza Ine kuitana olungama, koma ocimwa kuti atembenuke mtima,

33. Ndipo iwo anati kwa iye, Ophunzira a Yohane amasala kudya kawiri kawiri, ndi kucita mapemphero; cimodzimodzinso iwo a Afarisi; koma anu amangokudya ndi kumwa.

34. Koma Yesu anati kwa iwo, Kodi mungathe kuletsa anyamata a ukwati asadye, pamene mkwati ali nao pamodzi?

35. Koma masiku adzafika; ndipo pamene mkwati adzacotsedwa kwa iwo, pamenepo adzasala kudya masiku omwewo.

36. Ndipo iye ananenanso fanizo kwa iwo, kuti, Palibe munthu ang'amba cigamba ca maraya arsopano, naciphatika pa maraya akale; cifukwa ngati atero, angong'ambitsa atsopanowo, ndi cigamba ca atsopanowo sicidzayenerana ndi akalewo.

Werengani mutu wathunthu Luka 5