Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 12:33-53 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zacifundo; mudzikonzere matumba a ndarama amene sakutha, cuma cosatha m'Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.

34. Pakuti kumene kuli cuma canu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.

35. Khalani odzimangira m'cuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;

36. ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kucokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.

37. Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'cuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.

38. Ndipo akadza ulonda waciwiri, kapena wacitatu, nakawapeza atero, odala amenewa.

39. Koma zindikirani ici, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yace yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yace ibooledwe.

40. Khalani okonzeka inunso; cifukwa nthawi imene simulingirira, Mwana wa munthu akudza.

41. Ndipo Petro anati, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse?

42. Ndipo Ambuye anati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wace adzamuika kapitao wa pa banja lace, kuwapatsa iwo phoso lao pa nthawi yace?

43. Wodala kapoloyo amene mbuye wace pakufika, adzampeza alikucita cotero.

44. 1 Ndinena ndinu zoona, kuti adzamuika iye kapitao wa pa zonse ali nazo.

45. Koma 2 kapolo uyo akanena mumtima mwace, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;

46. 3 mbuye wa kapolouyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera, ndi nthawi yakuti saidziwa, nadzamdula iye pakati, nadzamuika dera lace pamodzi ndi anthu osakhulupirira.

47. Ndipo 4 kapolo uyo, wodziwa cifuniro ca mbuye wace, ndipo sanakonza, ndi kusacita zonga za cifuniro caceco, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri.

48. Koma 5 iye amene sanacidziwa, ndipo anazicita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu ali yense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.

49. Ine ndinadzera kuponya mota pa dziko lapansi; ndipo ndifunanji, ngati unatha kuyatsidwa?

50. Koma ndiri ndi ubatizo ndikabatizidwe nao; ndipo ndikanikizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa!

51. Kodi muyesa kuti ndinadzera kudzapatsa mtendere pa dziko lapani? Ndinena wa inu, Iaitu, komatu kutsutsana;

52. pakuti 6 kuyambira tsopano adzakhala m'nyumba imodzi anthu asanu, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu.

53. Adzatsutsana atate ndi mwana wace, ndi mwana ndi atate wace; amace adzatsutsana ndi mwana wamkazi'l ndi mwana wamkazi ndi amace, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wace, ndi mkaziyo ndi mpongozi wace.

Werengani mutu wathunthu Luka 12