Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 11:14-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo analikuturutsa ciwanda cosalankhula. Ndipo kunali, citaturuka ciwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa.

15. Koma ena mwa iwo anati, Ndi Beelzebule mkuru wa ziwanda amaturutsa ziwanda.

16. Koma ena anamuyesa, nafuna kwa iye cizindikilo cocokera Kumwamba.

17. Koma iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uli wonse wogawanika m'kati mwace upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m'kati mwace igwa.

18. Ndiponso ngati Satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wace? popeza munena kuti nditurutsa ziwanda ndi Beelzebule.

19. Koma ngati Ine ndimaturutsa ziwanda ndi Beelzebule, ana anu aziturutsa ndi yani? Mwa ici iwo adzakhala oweruza anu.

20. Koma ngati Ine nditurutsa ziwanda ndi cala ca Mulungu, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu.

21. Pamene pali ponse mwini mphamvu alonda pabwalo pace zinthu zace ziri mumtendere;

22. koma pamene pali ponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamlaka, amcotsera zida zace zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zace.

23. Iye wosabvomerezana ndi Ine atsutsana ndi Ine; ndipo iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwaza.

24. Pamene pali ponse mzimu wonyansa ukaturuka mwa munthu, upyola malo opanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera kunyumba kwanga kumene ndinaturukako;

25. ndipo pofika, uipeza yosesa ndi yokonzeka.

26. Pomwepo, upita nutenga mizimu yina isanu ndi iwiri yoipa yoposa ndi uwu mwini; ndipo ilowa nikhalira komweko; ndipo makhalidwe otsiriza a munthu uyu aipa koposa oyambawo.

27. Ndipo kunali, pakunena izi iye, mkazi wina mwa khamu la anthu anakweza mau, nati kwa iye, Yodala mimba imene idakubalani, ndi mawere amene munayamwa.

28. Koma iye anati, Inde, koma odala iwo akumva mau a Mulungu, nawasunga.

29. Ndipo pakusonkhana pamodzi makamu a anthu, anayamba kunena, Mbadwo uno ndi mbadwo woipa; ufuna cizindikilo, ndipo cizindikilo sicidzapatsidwa kwa uwu koma cizindikilo ca Yona.

30. Pakuti monga ngati Yona anali cizindikilo kwa Anineve, cotero adzakhalanso Mwana wa munthu kwa mbadwo uno.

31. Mfumu yaikazi ya kumwera idzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi amuna a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti anadza ku'cokera ku malekezero a dziko kudzamva nzeru za Solomo; ndipo onani, woposa Solomo ali pano.

32. Amuna a ku Nineve adzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti iwo analapa pa kulalikira kwa Y ona; ndipo onani, wakuposa Y ona ali pano.

33. Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m'cipinda capansi, kapena pansi pa muyeso, koma pa coikapo cace, kuti iwo akulowamo aone kuunika.

Werengani mutu wathunthu Luka 11