Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 14:7-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. koma lidzakhala tsiku la pa lokha lodziwika ndi Yehova; palibe usana, palibe usiku; koma kudzatero kuti madzulo kudzati mbe.

8. Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzaturuka ku Yerusalemu; gawo lao lina kumka ku nyanja ya kum'mawa, ndi gawo lina kumka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu.

9. Ndipo Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse; tsiku lomwelo Yehova adzakhala Iye yekha, ndi dzina lace ilo lokha.

10. Dziko lonse lidzasandulika, lidzanga cidikha, kuyambira ku Geba kufikira ku Rimoni, kumwela kwa Yerusalemu; ndipo pali uwupo padzakhala ponyamuka, ndipo udzakhala m'malo mwace, kuyambira ku cipata ca Benjamini kufikira ku malo a cipata coyamba, kufikira ku cipata ca kungondya, ndi kuyambira nsanja ya Hananeli kufikira ku zoponderamo mphesa za mfumu.

11. Ndipo anthu adzakhala m'menemo, ndipo sipadzakhalanso kuonongetsa; koma Yerusalemu adzakhala mosatekeseka.

12. Ndipo mliri umene Yehova adzakantha nao mitundu yonse ya anthu imene idathira nkhondo pa Yerusalemu ndi uwu: nyama yao idzaonda akali ciriri pa mapazi ao, ndi maso ao adzapuala m'pfunkha mwao, ndi lilime lao lidzanyala m'kamwa mwao.

13. Ndipo kudzali tsiku lomwelo, kuti cisokonezo cacikuru cocokera kwa Yehova cidzakhala pakati pao; ndipo adzagwira yense dzanja la mnzace; ndi dzanja lace lidzaukira dzanja la mnzace.

14. Ndi Yuda yemwe adzacita nkhondo ku Yerusalemu; ndi zolemera za amitundu onse ozungulirapo zidzasonkhanizidwa, golidi, ndi siliva, ndi zobvala zambirimbiri.

15. Momwemonso mliri wa pa akavalo, nyuru, ngamila, ndi aburu, ndi nyama zonse zokhala m'misasa iyo, udzakhala ngati mliri uwo.

16. Ndipo kudzacitika kuti otsala onse a amitundu onse anadzawo kulimbana ndi Yerusalemu, adzakwera caka ndi caka kulambira mfumu Yehova wa makamu, ndi kusunga madyerero amisasa.

17. Ndipo kudzacitika kuti ali yense wa mabanja a dziko wosakwera kumka ku Yerusalemu kulambira mfumu Yehova wa makamu, pa iwowa sipadzakhala mvula.

18. Ndipo banja la ku Aigupto likapanda kukwera, losafika, sirdzawagwera kodi mliri umene Yehova adzakantha nao amitundu osakwera kusunga madyerero amisasa?

19. Ili ndi cimo la Aigupto, ndi cimo la amitundu onse osakwerako kusunga madyerero a misasa.

20. Tsiku lomwelo padzaoneka pa miriu ya akavalo OPATULIKIRA YEHOVA; ndi mbiya za m'nyumba ya Yehova zidzanga mbale za ku guwa la nsembe.

21. Inde mbiya zonse za m'Yerusalemu ndi m'Yuda zidzakhala zopatulikira Yehova wa makamu; ndi onse akuphera nsembe adzafika nadzatengako, ndi kuphikamo; ndipo tsiku lomwelo simudzakhalanso Mkanani m'nyumba ya Yehova wa makamu.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 14