Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Ukulu wa Israyeli m'tsogolo

1. Katundu wa mau a Yehova wakunena Israyeli.Atero Yehova, wakuyala miyamba, ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kulenga mzimu wa munthu m'kati mwace;

2. Taonani, ndidzaika Yerusalemu akhale cipanda codzandiritsa kwa mitundu yonse ya anthu yozungulirapo, ndipo cidzafikira Yuda yemwe pomangira misasa Yerusalemu.

3. Ndipo kudzacitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndi amitundu onse a pa dziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao.

4. Tsiku ilo, ati Yehova, ndidzakantha kavalo ali yense ndi kumdabwitsa, ndi womkwera adzayaluka; ndipo ndidzatsegulira maso anga nyumba ya Yuda, ndi kukantha kavalo ali yense wa mitundu ya anthu akhale wakhungu.

5. Ndipo akalonga a Yuda adzanena m'mtima mwao, Okhala m'Yerusalemu ndiwo mphamvu yanga m'Yehova wa makamu Mulungu wao.

6. Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, ku dzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwace, m'Yerusalemu.

7. Ndipo Yehova adzayamba kupulumutsa mahema a Yuda, kuti ulemerero wa nyumba ya Davide ndi ulemerero wa okhala m'Yerusalemu usakulire Yuda.

8. Tsiku ilo Yehova adzacinjiriza okhala m'Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao.

9. Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, ndidzayesa kuononga amitundu onse akudza kuyambana ndi Yerusalemu.

10. Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala m'Yerusalemu, mzimu wa cisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wace mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wace woyamba.

11. Tsiku lomwelo kudzakhala maliro akuru m'Yerusalemu, ngati maliro a Hadadirimoni m'cigwa ca Megidoni,

12. Ndipo dziko lidzalira, banja liri lonse pa lokha; banja la nyumba ya Davide pa lokha, ndi akazi ao pa okha; banja la nyumba ya Natani pa lokha, ndi akazi ao pa okha;

13. banja la nyumba ya Levi pa lokha, ndi akazi ao pa lokha; banja la Asimei pa okha, ndi akazi ao pa okha;

14. mabanja onse otsala, banja liri lonse pa lokha, ndi akazi ao pa okha.