Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Masomphenya acisanu ndi cimodzi: mpukutu wouluka

1. Pamenepo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, taonani, mpukutu wouluka.

2. Ndipo anati kwa ine, Uona ciani? Ndipo ndinayankha, Ndiona mpukutu wouluka; utali wace mikono makumi awiri, ndi citando cace mikono khumi.

3. Ndipo anati kwa ine, Ili ndi temberero lirikuturukira pa dziko lonse; pakuti ali yense wakuba adzapitikitsidwa kuno monga mwa ili; ndi ali yense wakulumbira zonama adzapitikitsidwa kuno monga mwa ili.

4. Ndidzaliturutsa ili, ati Yehova wa makamu, ndipo lidzalowa m'nyumba ya wakuba, ndi m'nyumba ya iye wolumbira monama pa dzina langa; ndipo lidzakhala pakati pa nyumba yace, ndi kuitha pamodzi ndi mitengo yace ndi miyala yace.

Masomphenya acisanu ndi ciwiri: mkazi ndi efa

5. Pamenepo mthenga wakulankhula ndi ine anaturuka, nati kwa ine, Kwezatu maso ako, nuone ngati nciani ici cirikuturukaci.

6. Ndipo ndinati, Nciani ici? Nati iye, Ici ndi efa alikuturuka. Natinso, Ici ndi maonekedwe ao m'dziko lonse;

7. (ndipo taonani, cozunguniza cantobvu cotukulidwa) ndipo ici ndi mkazi wokhala pakati pa efa.

8. Ndipo anati, Uyu ndi ucimo; namgwetsa m'kati mwa efa; naponya ntobvu wolemerawo pakamwa pace.

9. Pamenepo ndinakweza maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anaturuka akazi awiri, ndi m'mapiko mwao munali mphepo; ndipo anali nao mapiko ngati mapiko a cumba, nanyamula efayo pakati pa dziko ndi thambo.

10. Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Amenewa amuka naye kuti efayo?

11. Ndipo anati kwa ine, Kummangira nyumba m'dziko la Sinara; kuti amuike, namkhazikeko pa kuzika kwace.