Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Malonjezo a kwa Israyeli

1. Pemphani kwa Yehova mvula, m'nyengo ya mvula ya masika, kwa Yehova wolenga mphezi; ndipo adzawapatsa mibvumbi ya mvula, kwayense zophukira kuthengo.

2. Pakuti aterafi anena zopanda pace, ndi aula aona bodza; nafotokoza maloto acabe, asangalatsa nazo zopanda pace; cifukwa cace ayendayenda ngati nkhosa, azunzika popeza palibe mbusa.

3. Mkwiyo wanga wayakira abusa, ndipo ndidzalanga atonde; pakuti Yehova wa makamu adzazonda zoweta zace, ndizo nyumba ya Yuda, nadzaziika ngati kavalo wace waulemerero kunkhondo.

4. Kwa iye kudzafuma mwala wa kungondya, kwa iye msomali, kwa iye uta wankhondo, kwa iye osautsa onse pamodzi.

5. Ndipo adzakhala ngati ngwazi zakupondereza adani m'thope la kubwalo kunkhondo; ndipo adzacita nkhondo, cifukwa Yehova ali nao; ndi apakavalo adzacitidwa manyazi.

6. Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawacitira cifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataya konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera.

7. Ndipo iwo a ku Efraimu adzakhala ngati ngwazi, ndi mtima wao udzakondwera ngati ndi vinyo; ndipo ana ao adzaciona nadzakondwera; mtima wao udzakondwerera mwa Yehova.

8. Ndidzawayimbira mluzu ndi kuwasonkhanitsa, pakuti ndawaombola; ndipo adzacuruka monga anacurukira kale.

9. Ndipo ndidzawafesa mwa mitundu ya anthu, ndipo adzandikumbukila m'maiko akutali; nadzakhala pamodzi ndi ana ao, nadzabwera.

10. Ndidzawatenganso ku dziko la Aigupto, ndi kuwasonkhanitsa m'Asuri; ndipo ndidzalowa nao m'dziko la Gileadi ndi Lebano; koma sadzawafikira.

11. Ndipo adzapita pakati pa nyanja ya nsautso, nadzapanda mafunde a m'nyanja, ndi maiwe onse a mtsinje adzaphwa; ndi kudzikuza kwa Asuri kudzagwetsedwa; ndi ndodo yacifumu ya Aigupto idzacoka.

12. Ndipo ndidzawalimbitsa mwa Yehova; ndipo adzayendayendam'dzina lace, ati Yehova.