Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Kuyeretsedwa kwa Yerusalemu

1. Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala m'Yerusalemu kasupe wa kwa ucimo ndi cidetso.

2. Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m'dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzacotsa m'dziko aneneri ndi mzimu wacidetso.

3. Ndipo kudzacitika, akaneneranso wina, atate wace ndi mai wace ombala adzanena naye, Sudzakhala ndi moyo, pakuti unena bodza m'dzina la Yehova; ndipo atate wace ndi mai wace ombala adzamgwaza ponenera iye.

4. Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo kuti aneneri adzacita manyazi yense ndi masomphenya ace, ponenera iye; ndipo sadzabvala copfunda caubweya kunyenga naco;

5. koma adzati, Sindiri mneneri, ndiri wolima munda; pakuti munthu anandiyesa kapolo kuyambira ubwana wanga.

6. Ndipo wina akati kwa iye, Zipsera izi m'manja mwako nza ciani? adzayankha, Ndizo za mabala anandilasa m'nyumba ya ondikonda.

7. Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.

8. Ndipo kudzacitika m'dziko lonse, ati Yehova, magawo awiri m'menemo adzalikhidwa nadzafa; koma gawo lacitatu lidzasiyidwa m'mwemo.

9. Ndi gawo lacitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golidi; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.