Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 8:13-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Momwemo anaika anthu, khamu lonse lokhala kumpoto kwa mudzi, ndi olalira ao kumadzulo kwa mudzi, ndipo usiku uja Yoswa analowa pakati pa cigwa,

14. Ndipo kunali, pamene mfumu ya ku Ai anaciona, anafulumira iwo, nalawira mamawa, naturuka amuna a m'mudzi kuthirana ndi Israyeli, iye ndi anthu ace onse, poikidwiratu patsogolo pa cidikha; popeza sanadziwa kuti amlalira kukhonde kwa mudzi.

15. Ndipo Yoswa ndi Aisrayeli onse anaoneka ngati a ku Ai alikuwathyola, nathawira njira ya kucipululu.

16. Pamenepo anthu onse okhala m'mudzi, anaitanidwa awapitikitse, nampitikitsa Yoswa, nakokedwa kusiyana ndi mudzi.

17. Ndipo sanatsala mwamuna mmodzi yense m'Ai kapena m'Beteli osaturukira kwa Israyeli; nasiya mudzi wapululu, napitikitsa Israyeli.

18. Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Tambasula nthungo iri m'dzanja lako iloze ku Ai, pakuti ndidzaupereka m'dzanja lako. Ndipo Yoswa anatambasula nthungoyo inali m'dzanja lace kuloza mudzi.

19. Nauka msanga olalirawo m'mbuto mwao, nathamanga pamene anatambasula dzanja lace, nalowa m'mudzi, naugwira; nafulumira nayatsa mudziwo.

20. Pamene amuna a ku Ai anaceuka, anapenya, ndipo taonani, utsi wa mudzi unakwera kumwamba; nasowa mphamvu iwo kuthawa cakuno kapena cauko; ndi anthu othawira kucipululu anatembenukira owapitikitsa.

21. Ndipo pakupenya Yoswa ndi Israyeli yense kuti olalirawo adagwira mudzi, ndi kuti utsi wa mudzi unakwera, anabwerera, nawapha amuna a ku Ai.

22. A kumudzinso anawaturukira; potero anakhala pakati pa Israyeli, ena mbali yina, ena mbali yina; ndipo anawakantha, mpaka sanatsala kapena kupulumuka wa iwo ndi mmodzi yense.

23. Koma mfumu ya ku Ai anamgwira wamoyo, nadza naye kwa Yoswa.

24. Ndipo kunali, atatha Israyeli kupha nzika zonse za ku Ai, kuthengo, kucipululu kumene anawapitikitsira, natha onse kugwa ndi lupanga lakuthwa mpaka adathedwa onse, Aisrayeli onse anabwerera ku Ai, naukantha ndi lupanga lakuthwa.

25. Ndipo onse amene adagwa tsiku lija, amuna ndi akazi, ndiwo zikwi khumi ndi ziwiri, anthu onse a ku Ai.

26. Popeza Yoswa sanabweza dzanja lace limene anatambasula nalo nthungo, mpaka ataononga konse nzika zonse za ku Ai.

27. Koma ng'ombe ndi zofunkha za mudzi uwu Israyeli anadzifunkhira monga mwa mau a Yehova amene analamulira Yoswa.

28. Ndipo Yoswa anatentha Ai, nausandutsa muunda ku nthawi yonse, bwinja kufikira lero lino.

29. Ndipo mfumu ya ku Ai, anampacika pamtengo mpaka madzulo; koma polowa dzuwa Yoswa analamulira kuti atsitse mtembo wace pamtengo; ndipo anauponya polowera pa cipata ca mudzi; nauniikako mulu waukuru wamiyala, mpaka lero lino.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 8