Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 5:6-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pakuti ana a Israyeli anayenda m'cipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo oturuka m'Aigupto udatha, cifukwa ca kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci.

7. Koma ana ao amuna amene anawautsa m'malo mwao, iwowa Yoswa anawadula; popeza anakhala osadulidwa, pakuti sanawadula panjira.

8. Ndipo kunali, atatha kudula mtundu wonse, anakhala m'malo mwao m'cigono mpaka adacira.

9. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero Uno ndakukunkhunizirani mtonzo wa Aigupto, Cifukwa cace dzina la malowo analicha Giligala kufikira lero lino.

10. Ndipo ana a Israyeli anamanga misasa ku Giligala; nacita Paskha tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi, madzulo, m'zidikha za Yeriko.

11. Ndipo m'mawa mwace atatha Paskha, anadya tirigu wakhwimbi wa m'dziko, mikate yopanda cotupitsa ndi tirigu wokazinga tsiku lomwe lija.

12. Koma m'mawa mwace mana analeka, atadya iwo tirigu wakhwimbi wa m'dziko; ndipo ana a Israyeli analibenso mana; koma anadya zipatso za dziko la Kanani caka comwe cija.

13. Ndipo kunali, pokhala Yoswa ku Yeriko, anakweza maso ace, napenya, ndipo taona, panaima muthu pandunji pace ndi lupanga lace losolola m'dzanja lace; namuka Yoswa kuli iye, nati iye, Ubvomerezana ndi ife kapena ndi aelani athu?

14. Nati, lai, koma ndadza ine, kazembe wa ankhondo a Yehova. Pamenepo Yoswa anagwa nkhope yace pansi, napembedza, nati kwa iye, Anenanji Ambuyanga kwa mtumiki wace?

15. Ndipo kazembe wa ankhondo a Yehova anati kwa Yoswa, Bvula nsapato yako pa phazi lako; pakuti malo upondapo mpopatulika. Nacita Yoswa comweco.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 5