Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 11:4-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo anaturuka, iwo ndi makamu ao onse nao, anthu ambiri, kucuruka kwao ngati mcenga uli m'mphepete mwa nyanja; ndi akavalo ndi magareta ambirimbiri.

5. Ndipo mafwnu awa onse anasonkhana, nadza namanga pamodzi ku madzi a Meromu, kumthira Israyeli nkhondo.

6. Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope cifukwa ca iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israyeli; uziwadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agareta ao ndi moto.

7. Ndipo Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo naye, anawadzera modzidzimutsa ku madzi a Meromu, nawagwera.

8. Ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Israyeli, ndipo anawakantha, nawapitikitsa mpaka ku Zidoni waukulu, ndi ku MiseripotuMaimu, ndi ku cigwa ca Mizepe kum'mawa; nawakantha mpaka sanawasiyira ndi mmodzi yense.

9. Ndipo Yoswa anawacitira monga Yehova adamuuza: nadula akavalo ao mitsindo, natentha magareta ao ndi moto.

10. Ndipo Yoswa anabwerera m'mbuyo nthawi imeneyi nalanda Hazori nakantha mfumu yace ndi lupanga; pakuti kale Hazori unali waukuru wa maufumu aja onse.

11. Ndipo anakantha amoyo onse anali m'mwemo, ndi lupanga lakuthwa, ndi kuwaononga konse, osasiyapo ndi mmodzi yense wakupuma mpweya; ndipo anatentha Hazori ndi moto.

12. Ndipo Yoswa analanda midzi yonse ya mafumu awa, ndi mafumu ao omwe nawakantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse; monga Mose mtumiki wa Yehova adalamulira.

13. Koma midzi yonse yomangidwa pa zitunda zao Israyeli sanaitentha, koma wa Hazori wokha; wnenewu Yoswa anautentha.

14. Ndi zofunkha zonse za midzi iyi ndi ng'ombe ana a Israyeli anadzifunkhira; koma anakantha ndi lupanga lakuthwa anthu onse mpaka adawaononga osasiyapo ndi mmodzi yense wopuma mpweya.

15. Monga Yehova adalamulira Mose mtumiki wace, momwemo Mose analamulira Yoswa; momwemonso anacita Yoswa; sanacotsapo mau amodzi pa zonse Yehova adalamulira Mose.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 11