Ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Israyeli, ndipo anawakantha, nawapitikitsa mpaka ku Zidoni waukulu, ndi ku MiseripotuMaimu, ndi ku cigwa ca Mizepe kum'mawa; nawakantha mpaka sanawasiyira ndi mmodzi yense.