Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 10:27-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo kunali, nthawi yakulowa dzuwa, Yoswa analamulira kuti awatsitse kumitengo; ndipo anawataya m'phanga m'mene adabisala; naika miyala yaikuru pakamwa pa phanga, mpaka lero lomwe lino.

28. Ndipo Yoswa anagwira Makeda tsiku lomwe lija ndi kuukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yace yom we; anawaononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, nacitira mfumu ya ku Makeda monga anacitira mfumu ya ku Yeriko.

29. Pamenepo Yoswa ndi Aisrayeli onse naye anapitirira kucokera ku Makeda kumka ku Libina, nathira nkhondo pa Libina;

30. ndipo Yehova anapereka uwunso, ndi mfumu yace m'dzanja la Israyeli; ndipo anaukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyamo ndi mmodzi yense; namcitira mfumu yace monga anacitira mfumu ya ku Yeriko.

31. Ndipo Yoswa, ndi Aisrayeli onse naye, anapitirira kucokera ku Libina kumka ku Lakisi; namanga misasa, nathira nkhondo pa uwo;

32. napereka Yehova Lakisi m'dzanja la Israyeli, ndipo anaulanda tsiku laciwiri, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo monga mwa zonse anacitira Libina.

33. Pamenepo Horamu mfumu ya Gezere anakwera kudzathandiza Lakisi; ndipo Yoswa anamkantha iye ndi anthu ace mpaka sanamsiyira ndi mmodzi yense.

34. Ndipo Yoswa, ndi Aisrayeli onse naye, anapitirira kucokera ku Lakisi mpaka ku Egiloni; namanga nrisasa, nathira nkhondo.

35. Naulanda tsiku lomwelo, naukantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse amoyo onse anali m'mwemo tsiku lomwelo, monga mwa zonse anacitira Lakisi.

36. Ndipo Yoswa ndi Aisrayeli onse naye anakwera kucokera ku Egiloni mpaka ku Hebroni, nauthira nkhondo;

37. naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yace ndi midzi yace yonse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, monga mwa zonse anacitira Egiloni; koma anauononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo.

38. Pamenepo Yoswa, ndi Aisrayeli onse naye, anabwerera kudza ku Dibiri, nauthira nkhondo,

39. naulanda, ndi mfumu yace ndi midzi yace yonse; naikantha ndi lupanga lakuthwa, naononga konse amoyo onse anali m'mwemo; sanasiya ndi mmodzi yense; monga anacitira Hebroni momwemo anacitira Dibiri ndi mfumu yace, monganso anacitira Libina ndi mfumu yace.

40. Motero Yoswa anakantha dziko lonse, la kumapiri, la kumwela, la kucidikha, la kuzigwa, ndi mafumu ao onse; sanasiyapo ndi mmodzi yense; koma anaononga psiti zonse zampweya, monga Yehova Mulungu wa Israyeli adalamulira.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 10