Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 10:19-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. koma inu musaime, pitikitsani adani anu, ndi kukantha a m'mbuyo mwao; musawalole alowe m'midzi mwao; pakuti Yehova Mulungu wanu anawapereka m'dzanja lanu.

20. Ndipo kunali, Yoswa ndi ana a Israyeli atatha kuwakantha, makanthidwe akurukuru mpaka atatha psiti, ndipo otsala a iwo atalowa m'midzi ya malinga,

21. anthu onse anabwerera kucigono kwa Yoswa pa Makeda ndi mtendere. Palibe munthu anacitira cipongwe mmodzi yense wa ana a Israyeli.

22. Pamenepo Yoswa anati, Tsegula pakamwa pa phanga ndi kunditurutsira m'phanga mafumu asanuwo.

23. Ndipo anatero, naturutsira m'phanga mafumu asanuwo, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yarimutu, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni.

24. Ndipo kunali, ataturutsira Yoswa mafumu awa, Yoswa anaitana amuna onse a Israyeli, ndipo anati kwa akazembe a anthu a nkhondo amene anamuka naye, Yandikirani, pondani pa makosi a mafumu awa. Nayandikira iwo, naponda pa makosi ao.

25. Pamenepo Yoswa ananena nao, Musaope, musatenge nkhawa; khalani amphamvu, nimulimbike mtima; pakuti Yehova adzatero ndi adani: anu onse amene mugwirana nao: nkhondo.

26. Ndipo atatero, Yoswa anawakantha nawapha, nawapacika pa mitengo isanu; nalikupacikidwa pa mitengo mpaka madzulo.

27. Ndipo kunali, nthawi yakulowa dzuwa, Yoswa analamulira kuti awatsitse kumitengo; ndipo anawataya m'phanga m'mene adabisala; naika miyala yaikuru pakamwa pa phanga, mpaka lero lomwe lino.

28. Ndipo Yoswa anagwira Makeda tsiku lomwe lija ndi kuukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yace yom we; anawaononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, nacitira mfumu ya ku Makeda monga anacitira mfumu ya ku Yeriko.

29. Pamenepo Yoswa ndi Aisrayeli onse naye anapitirira kucokera ku Makeda kumka ku Libina, nathira nkhondo pa Libina;

30. ndipo Yehova anapereka uwunso, ndi mfumu yace m'dzanja la Israyeli; ndipo anaukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyamo ndi mmodzi yense; namcitira mfumu yace monga anacitira mfumu ya ku Yeriko.

31. Ndipo Yoswa, ndi Aisrayeli onse naye, anapitirira kucokera ku Libina kumka ku Lakisi; namanga misasa, nathira nkhondo pa uwo;

32. napereka Yehova Lakisi m'dzanja la Israyeli, ndipo anaulanda tsiku laciwiri, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo monga mwa zonse anacitira Libina.

33. Pamenepo Horamu mfumu ya Gezere anakwera kudzathandiza Lakisi; ndipo Yoswa anamkantha iye ndi anthu ace mpaka sanamsiyira ndi mmodzi yense.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 10