Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 66:5-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ace; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja cifukwa ca dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi.

6. Mau a phokoso acokera m'mudzi, mau ocokera m'Kacisi, mau a Yehova amene abwezera adani ace cilango.

7. Mkazi asanamve zowawa, anabala mwana; kupweteka kwace kusanadze, anabala mwana wamwamuna.

8. Ndani anamva kanthu kotereko? ndani anaona zinthu zoterezo? Kodi dziko lidzabadwa tsiku limodzi? Kodi mtundu udzabadwa modzidzimutsa? pakuti pamene Ziyoni anamva zowawa, pomwepo anabala ana ace.

9. Kodi Ine ndidzafikitsira mkazi nthawi yakutula osamtulitsa? ati Yehova; kodi Ine amene ndibalitsa ndidzatseka mimba? ati Mulungu wako.

10. Sangalalani inu pamodzi ndi Yerusalemu, ndipo kondwani cifukwa ca iye, inu nonse amene mumkonda; sangalalani kokondwa pamodzi ndi iye, inu nonse akumlira maliro;

11. kuti mukayamwe ndi kukhuta ndi mabere a zitonthozo zace; kuti mukafinye mkaka ndi kukondwerera ndi unyinji wa ulemerero wace.

12. Pakuti atero Yehova, Taonani ndidzamfikitsira mtendere ngati mtsinje, ndi ulemerero wa amitundu ngati mtsinje wosefukira. Inu mudzayamwa, ndi kunyamulidwa pambali, ndi kululuzidwa pa maondo,

13. Monga munthu amene amace amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu; ndipo mudzatonthozedwa mtima m'Yerusalemu.

14. Ndipo mudzaciona, ndipo mtima wanu udzasangalala, ndipo mafupa anu adzakula ngati msipu; ndipo dzanja la Yehova lidzadziwika ndi atumiki ace, ndipo adzakwiyira adani ace.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 66