Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ace; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja cifukwa ca dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi.