Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 66:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wacifumu, ndi dziko lapansi ndi coikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?

2. Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.

3. Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwana wa nkhosa alingana ndi wotyola khosi la garu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza conunkhira akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zao zao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;

4. Inenso ndidzasankha zodzinyenga nazo, ndipo ndidzatengera mantha ao pa iwo; pakuti pamene ndinaitana, panalibe woyankha; pamene ndinalankhula, iwo sanamva konse; koma anacita coipa m'maso mwanga, ndi kusankha cimene ndisanakondwere naco.

5. Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ace; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja cifukwa ca dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi.

6. Mau a phokoso acokera m'mudzi, mau ocokera m'Kacisi, mau a Yehova amene abwezera adani ace cilango.

7. Mkazi asanamve zowawa, anabala mwana; kupweteka kwace kusanadze, anabala mwana wamwamuna.

8. Ndani anamva kanthu kotereko? ndani anaona zinthu zoterezo? Kodi dziko lidzabadwa tsiku limodzi? Kodi mtundu udzabadwa modzidzimutsa? pakuti pamene Ziyoni anamva zowawa, pomwepo anabala ana ace.

9. Kodi Ine ndidzafikitsira mkazi nthawi yakutula osamtulitsa? ati Yehova; kodi Ine amene ndibalitsa ndidzatseka mimba? ati Mulungu wako.

10. Sangalalani inu pamodzi ndi Yerusalemu, ndipo kondwani cifukwa ca iye, inu nonse amene mumkonda; sangalalani kokondwa pamodzi ndi iye, inu nonse akumlira maliro;

11. kuti mukayamwe ndi kukhuta ndi mabere a zitonthozo zace; kuti mukafinye mkaka ndi kukondwerera ndi unyinji wa ulemerero wace.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 66