Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 42:16-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa; m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu Izi ine ndidzacita, ndipo sindidzawasiya.

17. Iwo adzabwezedwa m'mbuyo, adzakhala ndi manyazi ambiri amene akhulupirira mafano osemedwa, nati kwa mafano oyengeka, Inu ndinu milungu yathu.

18. Imvani, agonthi inu; yang'anani, akhungu inu, kuti muone.

19. Ndani ali wakhungu, koma mtumiki wanga? pena wagonthi, monga mthenga wanga, amene ndimtumiza? ndani ali wakhungu monga bwenzi langa, ndi wakhungu monga mtumiki wa Yehova?

20. Iwe waona zinthu zambiri, koma susamalira konse; makutu ako ali otseguka, koma sumva konse.

21. Cinakondweretsa Yehova cifukwa ca cilungamo cace kukuza cilamulo, ndi kucilemekeza.

22. Koma awa ndiwo anthu olandidwa zao ndi kufunkhidwa; iwo onse agwa m'mauna, nabisidwa m'nyumba zakaidi; alandidwa zao, palibe wowapulumutsa; afunkhidwa ndipo palibe woti, Bwezerani.

23. Ndani mwa inu adzachera khutu lace pamenepo? amene adzamvera ndi kumva nthawi yakudza?

24. Ndani anapereka Yakobo, kuti afunkhidwe, ndi Israyeli, kuti awawanyidwe? kodi si Yehova? Iye amene tamcimwira, ndi amene iwo anakonda kuyenda m'njira zace, ngakhale kumvera ciphunzitso cace.

25. Cifukwa cace anatsanulira pa iye mkwiyo wace waukali, ndi mphamvu za nkhondo; ndipo unamyatsira moto kuzungulira kwace, koma iye sanadziwa; ndipo unamtentha, koma iye sanacisunga m'mtima.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 42