Cifukwa cace anatsanulira pa iye mkwiyo wace waukali, ndi mphamvu za nkhondo; ndipo unamyatsira moto kuzungulira kwace, koma iye sanadziwa; ndipo unamtentha, koma iye sanacisunga m'mtima.