Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 37:24-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Wamtonza Ambuye ndi atumiki ako, ndipo wati, Ndi khamu la magareta anga ine ndafika ku nsonga za mapiri, ku mbali za Lebano; ndipo ndidzagwetsapo mikungudza yaitali, ndi milombwa yosankhika; ndipo ine ndidzafika pamutu pace penipeni, ku nkhalango ya munda wace wobalitsa.

25. Ine ndakumba ndi kumwa madzi, ndidzaumitsa nyanja zonse za Aigupto ndi kuphazi kwanga.

26. Kodi iwe sunamve, kuti ndinacita ici kale, ndi kucikonza nthawi zakale? tsopano Ine ndacikwaniritsa, kuti iwe ukapasule midzi yamalinga, isanduke miunda.

27. Cifukwa cace okhalamo analefuka, naopsedwa, nathedwa nzeru; ananga udzu wa in'munda, ndi masamba awisi, ndi udzu wa pamacindwi, ndi munda wa tirigu asanakule.

28. Koma ndidziwa pokhala pansi pako, ndi kuturuka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundikwiyira kwako.

29. Cifukwa ca kundikwiyira Ine kwako, ndi popeza kudzikweza kwako kwafika m'makutu mwanga. Ine ndidzaika mbedza yanga m'mphuno mwako, ndi capakamwa canga m'milomo yako, ndipo ndidzakubweza iwe m'njira yomwe unadzerayo.

30. Ndipo ici cidzakhala cizindikilo kwa iwe: caka cino mudzadya zimene ziri zomera zokha, ndipo caka caciwiri mankhokwe ace; ndipo caka cacitatu bzalani ndi kudula ndi kulima minda yamphesa ndi kudya cipatso cace.

31. Ndipo otsala amene opulumuka a nyumba ya Yuda adzaphukanso mizu pansi, nadzabala cipatso pamwamba.

32. Pakuti mudzaoneka m'Yerusalemu, otsala ndi opulumuka m'Yerusalemu, otsala ndi opulumuka m'phiri la Ziyoni; cangu ca Yehova wa makamu cidzacita ici.

33. Cifukwa cace atero Yehova za mfumu ya Asuri, Iye sadzafika pa mudzi uno, ngakhale kuponyapo mubvi, ngakhale kufika patsogolo pace ndi cikopa, ngakhale kuunjikirapo mulu.

34. Pa njira yomwe anadzerayo, abwerera yomweyo, ndipo sadzafika pa mudzi uno, ati Yehova.

35. Pakuti ndidzacinjiriza mudzi uno, kuupulumutsa, cifukwa ca Ine mwini, ndi mtumiki wanga Davide.

36. Ndipo mthenga wa Yehova anaturuka, naphaipha m'zitando za Asuri, zikwi zana ndi makumi asanu ndi atatu ndi zisanu, ndipo pamene anthu anauka mamawa, taonani, onse ndiwo mitembo.

37. Ndipo Sanakeribu, mfumu ya Asuri, anacoka, namuka, nabwerera, nakhala pa Nineve,

38. Ndipo panali, pamene iye analikupembedzera m'nyumba ya Nisiroki, mulungu wace, Adrameleki ndi Sarezeri, ana ace anampha iye ndi lupanga; ndipo iwo anapulumuka, nathawira ku dziko la ku Ararati. Ndipo Esaradoni, mwana wace, analamulira m'malo mwace.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 37