Ndipo ici cidzakhala cizindikilo kwa iwe: caka cino mudzadya zimene ziri zomera zokha, ndipo caka caciwiri mankhokwe ace; ndipo caka cacitatu bzalani ndi kudula ndi kulima minda yamphesa ndi kudya cipatso cace.