Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 25:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo m'phiri limendi Yehova wa makamu adzakonzera anthu ace onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okha okha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.

7. Ndipo Iye adzaononga m'phiri limeneli cophimba nkhope cobvundikira mitundu yonse ya anthu, ndi nsaru yokuta amitundu onse.

8. Iye wameza imfa ku nthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo citonzo ca anthu ace adzacicotsa pa dziko lonse lapansi; cifukwa Yehova wanena.

9. Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndikusekereram'cipulumutso cace.

10. Cifukwa m'phiri limeneli dzanja la Yehova lidzakhalamo, ndipo Moabu adzaponderezedwa pansi m'malo ace, monga maudzu aponderezedwa padzala.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 25