Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 52:18-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndiponso miphika, ndi zoolera, ndi mbano zao, ndi mbale, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo, anazicotsa.

19. Ndi zikho, ndi zopalira moto, ndi mbale, ndi miphika, ndi zoikapo nyali, ndi zipande, ndi mitsuko; ndi golidi, wa zija zagolidi, ndi siliva, wa zija zasiliva, kapitao wa alonda anazicotsa.

20. Nsanamira ziwirizo, thawale limodzilo, ndi ng'ombe zamkuwa zinali pansi pa zoikapo, zimene mfumu Solomo anazipangira nyumba ya Yehova; mkuwa wa zipangizo zonsezi sanatha kuyesa kulemera kwace.

21. Koma nsanamirazo, utari wace wa nsanamira yina unafikira mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndi cingwe ca mikono khumi ndi iwiri cinaizinga; kucindikira kwace kunali zala zinai; inali yagweregwere.

22. Ndipo korona wamkuwa anali pamwamba pace; utari wace wa korona mmodzi unali wa mikono isanu, ndi made ndi makangaza pakorona pozungulira pace, onse amkuwa: nsanamira inzace yomwe inali nazo zonga zomwezi, ndi makangaza.

23. Ndipo pambali pace panali makangaza makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi limodzi; ndipo makangaza onse anali zana limodzi pamade pozungulira pace.

24. Ndipo kapitao wa alonda anatenga Seraya mkuru wansembe, ndi Zefaniya wansembe waciwiri, ndi akudikira pakhomo atatu;

25. ndipo m'mudzi anatenga kazembe amene anali woyang'anira anthu a nkhondo ndi amuna asanu ndi awiri a iwo akuona nkhope ya mfumu, amene anapezedwa m'mudzi; ndi mlembi wa kazembe wa nkhondo, amene akamemeza anthu a m'dziko; ndi amuna makumi asanu ndi limodzi a anthu a m'dziko, amene anapezedwa pakati pa mudzi.

26. Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga iwo, nadza nao kwa mfumu ya ku Babulo ku Ribila.

27. Ndipo mfumu ya ku Babulo anawakantha, nawapha pa Ribila m'dziko la Hamati. Comweco Yuda anatengedwa ndende kuturuka m'dziko lace.

28. Amenewa ndi anthu amene Nebukadirezara anatenga ndende: caka cacisanu ndi ciwiri, Ayuda zikwi zitatu kudza makumi awiri ndi atatu;

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 52