Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 51:3-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Wauta asakoke uta wace, asadzikweze m'malaya ace acitsulo; musasiye anyamata ace; muononge ndithu khamu lace lonse.

4. Ndipo adzagwa ophedwa m'dziko la Akasidi, opyozedwa m'miseu yace.

5. Pakuti Israyeli ndi Yuda sasiyidwa ndi Mulungu wao, ndiye Yehova wa makamu: ngakhale dziko lao ladzala ndi ucimo kucimwira Woyera wa Israyeli.

6. Thawani pakati pa Babulo, yense apulumuke moyo wace; musathedwe m'coipa cace; pakuti ndi nthawi ya kubwezera cilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yace.

7. Babulo wakhala cikho cagolidi m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wace; cifukwa cace amitundu ali ndi misala.

8. Babulo wagwa dzidzidzi naonongedwa; mumkuwire iye; mutengere zowawa zace bvunguti, kapena angacire.

9. Tikadaciritsa Babulo koma sanacire; mumsiye iye, tipite tonse yense ku dziko lace; pakuti ciweruziro cace cifikira kumwamba, cinyamulidwa mpaka kuthambo,

10. Yehova waturutsa cilungamo cathu; tiyeni tilalikire m'Ziyoni nchito ya Yehova Mulungu wathu.

11. Nolani mibvi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; cifukwa alingalirira Babulo kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera cilango kwa Yehova; kubwezera cilango cifukwa ca Kacisi wace.

12. Muwakwezere mbendera makoma a Babulo, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kucita comwe ananena za okhala m'Babulo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 51