Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 49:23-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Za Damasiko. Hamati ndi Aripadi ali ndi manyazi, cifukwa anamva malodza, asungunuka kunyanja, adera nkhawa osatha kukhala cete.

24. Damasiko walefuka, atembenukira kuti athawe, kunthunthumira kwamgwira; zobvuta ndi kulira zamgwira iye, ngati mkazi alimkudwala.

25. Alekeranji kusiya mudzi wa cilemekezo, mudzi wa cikondwero canga?

26. Cifukwa cace anyamata ace adzagwa m'miseu yace, ndipo anthu onse a nkhondo adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu.

27. Ndipo Ine ndidzayatsa moto m'khoma la Damasiko, udzathetsa zinyumba za Beni-Hadadi.

28. Za Kedara, ndi za maufumu a Hazori, amene anawakantha Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo.Yehova atero: Ukani, kwerani ku Kedara, funkhani ana a kum'mawa.

29. Mahema ao ndi zoweta zao adzazilanda, adzadzitengera nsaru zocingira zao, ndi katundu wao yense, ndi ngamila zao; ndipo adzapfuulira iwo, Mantha ponse ponse.

30. Thawani inu, yendani kutari, khalani mwakuya, Inu okhala m'Hazori, ati Yehova; pakuti Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anapangira uphungu pa inu, nakulingalirirani.

31. Nyamukani, kwererani mtundu wokhala ndi mtendere, wokhala osadera nkhawa, ati Yehova, amene alibe zitseko ndi mipiringidzo, okhala pa okha.

32. Ndipo ngamila zao zidzakhala zofunkha, ndi unyinji wa ng'ombe zao udzakhala wolanda; ndipo ndidzabalalitsira ku mphepo zonse iwo amene ameta m'mbali mwa tsitsi lao; ndipo ndidzatenga tsoka lao ku mbali zao zonse, ati Yehova.

33. Ndipo Hazori adzakhala mokhalamo ankhandwe, bwinja lacikhalire; simudzakhalamo munthu, simudzagonamo mwana wa munthu.

34. Mau a Yehova amene anafika kwa Yeremiya mneneri, onena za Elamu poyamba kulamulira Zedekiya mfumu ya Yuda, kuti,

35. Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatyola uta wa Elamu, ndiwo mtima wa mphamvu yao.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 49