Ndipo ngamila zao zidzakhala zofunkha, ndi unyinji wa ng'ombe zao udzakhala wolanda; ndipo ndidzabalalitsira ku mphepo zonse iwo amene ameta m'mbali mwa tsitsi lao; ndipo ndidzatenga tsoka lao ku mbali zao zonse, ati Yehova.