Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 44:15-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo amuna onse amene anadziwa kuti akazi ao anafukizira milungu yina, ndi akazi onse omwe anaimirirapo, msonkhano waukuru, anthu onse okhala m'dziko la Aigupto, m'Patirosi, anamyankha Yeremiya, kuti,

16. Koma mau amene wanena ndi ife m'dzina la Yehova, sitidzakumvera iwe.

17. Koma tidzacita ndithu mau onse anaturuka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tikacitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akuru athu, m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi cakudya cokwanira, tinakhala bwino, sitinaona coipa.

18. Koma cilekere ife kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, tasowa zonse, tathedwa ndi lupanga ndi caola.

19. Ndipo pamene tinafukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira nsembe zothira, kodi tinamuumbira iye mikate yakumpembedzera, ndi kumthirira nsembe zothira, opanda amuna athu?

20. Ndipo Yeremiya anati kwa anthu onse, kwa amuna, ndi kwa akazi, kwa anthu onse amene anambwezera mau amenewa, ndi kuti,

21. Zofukizira zanu m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, za inu ndi atate anu, mafumu anu ndi akuru anu, ndi anthu a m'dziko, kodi Yehova sanazikumbukira, kodi sizinalowa m'mtima mwace?

22. ndipo Yehova sanatha kupirirabe, cifukwa ca macitidwe anu oipa, ndi cifukwa ca zonyansa zimene munazicita; cifukwa cace dziko lanu likhala bwinja, ndi cizizwitso, ndi citemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe.

23. Cifukwa mwafukiza, ndi cifukwa mwacimwira Yehova, osamvera mau a Yehova, osayenda m'cilamulo cace, ndi m'malemba ace, ndi m'mboni zace, cifukwa cace coipaci cakugwerani, monga lero lomwe.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 44