Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 4:16-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira ku dziko lakutari, nainenera midzi ya Yuda mau ao.

17. Monga adindo a m'munda amzinga iye; cifukwa andipandukira Ine, ati Yehova.

18. Njira yako ndi nchito zako zinakucitira izi; ici ndico coipa cako ndithu; ciri cowawa ndithu, cifikira ku mtima wako.

19. Matumbo anga, matumbo anga! ndipoteka pamtima panga peni peni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.

20. Alalikira cipasuko cilalikire; pakuti dziko lonse lafunkhidwa; mahema anga afunkhidwa dzidzidzi, ndi nsaru zanga zocinga m'kamphindi.

21. Kufikira liti ndidzaona mbendera, ndi kumva kulira kwa lipenga?

22. Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ocenjera kucita coipa koma kucita cabwino sakudziwa.

23. Ndinaona dziko lapansi, ndi rpo taona, linali lopasuka lopanda kanthu; ndipo ndinaona kumwamba, kunalibe kuunika.

24. Ndinaona mapiri, taona ananthunthumira; ndipo zitunda zonse zinagwedezeka.

25. Ndinaona, ndipo taona, panalibe munthu, ndi mbalame zonse zakumwamba zinathawa.

26. Ndinaona, ndipo taona, munda wazipatso unali cipululu, ndipo midzi yace yonse inapasuka pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa mkwiyo wace woopsya.

27. Pakuti Yehova atero, Dziko lonse lidzakhala bwinja koma sindidzatsirizitsa.

28. Cifukwa cimeneco dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; cifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo.

29. Mudzi wonse uthawa m'phokoso la apakavalo ndi amauta; adzalowa m'nkhalango, adzakwera pamiyala; midzi yonse idzasiyidwa, ndipo simudzakhala munthu m'menemo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 4