Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 35:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti,

13. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Pita, nunene kwa anthu a Yuda ndi kwa okhala m'Yerusalemu, Kodi simudzalola kulangizidwa kumvera mau anga ati Yehova.

14. Mau a Yonadabu mwana wa Rekabu, amene anauza ana ace, asamwe vinyo, alikucitidwa, ndipo mpaka lero samamwa, pakuti amvera lamulo la kholo lao; koma Ine ndanena ndi inu, ndalawirira ndi kunena; koma simunandimvera Ine.

15. Ndatumanso kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndalawirira ndi kuwatuma, kuti, Bwererani kuleka yense njira yace yoipa, konzani macitidwe anu, musatsate milungu yina kuitumikira, ndipo mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu; koma simunandichera khutu lanu, simunandimvera Ine.

16. Pakuti monga ana a Yonadabu mwana wa Rekabu acita lamulo la kholo lao limene anawauza, koma anthu awa sanandimvera Ine.

17. Cifukwa cace atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani, ndidzafikitsa pa Yuda ndi pa onse okhala m'Yerusalemu coipa conseco ndawanenera iwo; cifukwa ndanena ndi iwo, koma sanamve; ndaitana, koma iwo sanandibvomera.

18. Ndipo Yeremiya anati kwa nyumba ya Arekabu, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Cifukwa mwamvera lamulo la Yonadabu kholo lanu, ndi kusunga zonse anakulangizani inu, ndi kucita monga mwa zonse anakuuzani inu;

19. cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Yonadabu mwana wa Rekabu sadzasowa munthu wakuima pamaso panga kumuyaya.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 35