Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 29:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo ndidzatsata iwe ndi lupanga, ndi njala, ndi caola, ndipo ndidzawapereka akhale oopsyetsa m'maufumu onse a dziko la pansi, akhale citemberero, ndi codabwitsa, ndi cotsonyetsa, ndi citonzo, kwa mitundu yonse kumene ndinawapitikitsirako;

19. cifukwa sanamvera mau anga, ati Yehova, amene ndinawatumizira ndi atumiki anga aneneri, ndi kuuka mamawa ndi kuwatuma, koma munakana kumva, ati Yehova.

20. Pamenepo tamvani inu mau a Yehova, inu nonse a m'ndende, amene ndacotsa m'Yerusalemu kunka ku Babulo.

21. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, za Ahabu mwana wace wa Koliya, ndi za Zedekiya mwana wace wa Maseya, amene anenera zonama m'dzina langa: Taonani, Ndidzawapereka m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo; ndipo Iye adzawapha pamaso panu;

22. ndipo am'nsinga onse a Yuda amene ali m'Babulo adzatemberera pali iwo, kuti, Yehova akucitire iwe monga Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babulo inaoca m'moto;

23. cifukwa anacita zopusa m'Israyeli, nacita cigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m'dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.

24. Ndipo za Semaya Mnehelamu uzinena, kuti,

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 29