Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 23:29-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Kodi mau anga safanafana ndi moto? ati Yehova, ndi kufanafana ndi nyundo imene iphwanya mwala?

30. Cifukwa cace, taonani, Ine ndidana ndi aneneri, ati Yehova, amene amaba mau anga, yense kumbera mnansi wace.

31. Taonani, Ine ndidana ndi aneneri, ati Yehova, amene acita ndi malilime ao, ndi kuti, Ati Iye.

32. Taonani, Ine ndidana ndi amene anenera maloto onama, ndi kuwafotokoza ndi kusokeretsa anthu anga ndi zonama zao, ndi matukutuku ao acabe; koma Ine sindinatuma iwo, sindinauza iwo; sadzapindulira konse anthu awa, ati Yehova.

33. Ndipo pamene anthu awa, kapena mneneri, kapena wansembe, adzakufunsa iwe, kuti, Katundu wa Yehova ndi ciani? pamenepo uziti kwa iwo, Katundu wanji? Ndidzakucotsani inu, ati Yehova.

34. Koma za mneneri, ndi wansembe, ndi anthu, amene adzati, Katundu wa Yehova, ndidzamlanga munthuyo ndi nyumba yace.

35. Mudzatero yense kwa mnansi wace, ndi yense kwa mbale wace, Yehova wayankha ciani? ndipo Yehova wanena ciani?

36. Ndipo katundu wa Yehova simudzachulanso konse; pakuti mau a munthu adzakhala katundu wace; pakuti mwasokoneza mau a Mulungu wamoyo, Yehova wa makamu, Mulungu wathu.

37. Uzitero kwa mneneri, Yehova wakuyankha ciani? ndipo Yehova wanenanji?

38. Koma ngati muti, Katundu wa Yehova, cifukwa cace Yehova atero: Cifukwa muti mau awa, Katundu wa Yehova, ndipo ndatuma kwa inu, kuti, Musati, Katundu wa Yehova;

39. cifukwa cace, taonani, ndidzakuiwalani inu konse, ndipo ndidzakucotsani, ndi mudzi umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, ndidzaucotsa pamaso panga;

40. ndipo ndidzakutengerani inu citonzo camuyaya, ndi manyazi amuyaya, amene sadzaiwalika.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 23