Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 22:6-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Gileadi, ndi mutu wa Lebano; koma ndidzakuyesa iwe cipululu, ndi midzi yosakhalamo anthu.

7. Ndipo ndidzakupangiratu iwe opasula, yense ndi zida zace; ndipo adzadula mikungudza yako yosankhika nadzaiponya m'moto.

8. Ndipo amitundu ambiri adzapita pa mudzi uwu, nadzati yense kwa mnzace, Yehova anatero nao mudzi waukuru uwu cifukwa ninji?

9. Ndipo adza yankha, Cifukwa anasiya pangano la Yehova Mulungu wao, ndi kugwadira milungu yina, ndi kuitumikira.

10. Musamlirire wakufa, musacite maliro ace; koma mumliritse iye amene amuka, pakuti sadzabweranso, kapena kuonanso dziko la kwao.

11. Pakuti Yehova atero za Salumu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene analamulira m'malo mwace mwa Yosiya atate wace, amene anaturuka m'malo muno: Sadzabweranso kuno nthawi iri yonse;

12. koma kumene anamtengera iye ndende, kumeneko adzafa, ndipo sadzaonanso dziko ili.

13. Tsoka iye amene amanga nyumba yace ndi cisalungamo, ndi zipinda zapamwamba ndi cosaweruza bwino; amene agwiritsa mnzace nchito osamlipira, osampatsa mphotho yace;

14. amene ati, Ndidzadzimangira ndekha nyumba yotakata ndi zipinda zapamwamba zazikuru, nadziboolera mazenera; nabvundima chindwi lam'kati ndi mikungudza, naipaka ndi utoto wofiira.

15. Kodi udzakhala mfumu, cifukwa iwe uyesa kuposa ena ndi mikungudza? Kodi atate wako sanadya ndi kumwa, ndi kuweruza molungama? kumeneko kunamkomera.

16. Iye anaweruza mlandu wa aumphawi ndi osowa; kumeneko kunali kwabwino. Kodi kumeneko si kundidziwa Ine? ati Ambuye.

17. Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosacimwa, ndi kusautsa, ndi zaciwawa, kuti uzicite.

18. Cifukwa cace Yehova atero za Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda: Sadzamlira iye, kuti, Kalanga ine mbale wanga! kapena, Kalanga ine mlongo wanga! Sadzamlira, kuti, Kalanga ine mbuye! kapena, Kalanga ine ulemerero wace!

19. Adzamuika monga kuika buru, adzamkoka nadzamponya kunja kwa zipata za Yerusalemu.

20. Kwera ku Lebano, nupfuule; kweza mau ako m'Basani; nupfuule m'Abarimu; pakuti mabwenzi ako onse atha,

21. Ndinanena ndi iwe m'phindu lako; koma unati, Sindidzamva. Awa ndi makhalidwe ako kuyambira ubwana wako, kuti sudamvera mau anga,

22. Mphepo idzadyetsa abusa ako onse, ndipo mabwenzi ako adzalowa m'ndende; ntheradi udzakhala ndi manyazi ndi kunyazitsidwa cifukwa ca coipa cako conse.

23. Iwe wokhala m'Lebano, womanga cisa cako m'mikungudza, udzacitidwa cisoni cacikuru nanga pamene mapweteko adzadza kwa iwe, monga mkazi alinkudwala!

24. Pali ine, ati Yehova, ngakhale Koniya mwana wace wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda akadakhala mphete ya pa dzanja langa lamanja, ndikadacotsa iwe kumeneko;

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 22