Pakuti Yehova atero za Salumu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene analamulira m'malo mwace mwa Yosiya atate wace, amene anaturuka m'malo muno: Sadzabweranso kuno nthawi iri yonse;