Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 20:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Pasuri mwana wace wa Imeri wansembe, amene anali kapitao wamkuru m'nyumba ya Yehova, anamva Yeremiya alikunenera zimenezi.

2. Ndipo Pasuri anampanda Yeremiya mneneriyo, namuika matangadza amene anali m'cipata ca kumtunda ca Benjamini, cimene cinali ku nyumba ya Yehova.

3. Ndipo panali m'mawa mwace, kuti Pasuri anaturutsa Yeremiya m'matangadzamo. Ndipo Yeremiya anati kwa iye, Yehova sanacha dzina lako Pasuri, koma Magorimisabibu.

4. Pakuti Yehova atero, Taonani, ndidzakuyesa iwe coopsa ca kwa iwe mwini, ndi kwa abale ako onse; ndipo iwo adzagwa ndi lupanga la adani ao, ndipo maso ako adzaona; ndipo ndidzapereka Ayuda onse m'dzanja la mfumu ya ku Babulo, ndipo iye adzawatengera iwo am'nsinga ku Babulo, nadzawapha ndi lupanga,

5. Ndiponso ndidzapereka cuma conse ca mudzi uwu, ndi zaphindu zace zonse, ndi zinthu zace zonse za mtengo wace, inde, zolemera zonse za mafumu a Yuda ndidzapereka m'manja mwa adani ao, amene adzazifunkha, nadzazitenga kunka nazo ku Babulo.

6. Ndipo iwe, Pasuri, ndi onse okhala m'nyumba mwako mudzanka kundende; ndipo udzafika ku Babulo, ndi pamenepo udzafa, ndi pamenepo udzaikidwa, iwe, ndi mabwenzi ako onse, amene unawanenera mabodza.

7. Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwalakika; ine ndikhala coseketsa dzuwa lonse, lonse andiseka.

8. Pakuti pali ponse ndinena, ndipfuula; ndipfuula, Ciwawa ndi cofunkha; pakuti mau a Mulungu ayesedwa kwa ine citonzo, ndi coseketsa, dzuwa lonse.

9. Ndipo ngati nditi, Sindidzamchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lace, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 20