Ndipo iwe, Pasuri, ndi onse okhala m'nyumba mwako mudzanka kundende; ndipo udzafika ku Babulo, ndi pamenepo udzafa, ndi pamenepo udzaikidwa, iwe, ndi mabwenzi ako onse, amene unawanenera mabodza.