Ndipo panali m'mawa mwace, kuti Pasuri anaturutsa Yeremiya m'matangadzamo. Ndipo Yeremiya anati kwa iye, Yehova sanacha dzina lako Pasuri, koma Magorimisabibu.