Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 15:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samueli akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwacotse iwo pamaso panga, aturuke.

2. Ndipo padzakhala, pamene adzati kwa iwe, Titurukire kuti? pamenepo uziti, Atero Yehova: Amene a kuimfa, anke kuimfa; amene a kulupanga, anke kulupanga; amene a kunjala, anke kunjala; ndi amene a kunsinga, anke kunsinga.

3. Ndipo ndidzaika pa iwo mitundu inai, ati Yehova, lupanga lakupha, agaru akung'amba, mbalame za m'mlengalenga, ndi zirombo zapansi, zakulusa ndi kuononga.

4. Ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, cifukwa ca Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda, cifukwa ca zija anacita m'Yerusalemu.

5. Pakuti ndani adzakucitira iwe cisoni, Yerusalemu? ndani adzakulirira iwe? ndani adzapatukira kudzafunsa za mkhalidwe wako?

6. Iwe wandikana Ine, ati Yehova, wabwerera m'mbuyo; cifukwa cace ndatambasulira dzanja langa pa iwe, ndi kukuononga iwe; ndatopa ndi kulekerera.

7. Ndawakupa ndi mkupo m'zipata za dziko; ndacotsa ana ao, ndasakaza anthu anga; sanabwerere kuleka njira zao.

8. Amasiye ao andicurukira Ine kopambana mcenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha.

9. Mkazi amene anabala asanu ndi awiri walefuka; wapereka moyo; dzuwa lace lalowa usana ulipobe; wanyazitsidwa, wathedwa nzeru; otsala ao ndidzapereka kulupanga pamaso pa adani ao, ati Yehova.

10. Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletsa paphindu; koma iwo onse anditemberera.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 15