Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 14:9-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, tichedwa ndi dzina lanu; musatisiye.

10. Atero Yehova kwa anthu awa, Comwecoakonda kusocerera; sanakaniza mapazi ao; cifukwa cace. Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira coipa cao, nadzalanga zocimwa zao.

11. Ndipo Yehova anati kwa ine, Usapempherere anthu awa zabwino.

12. Pamene asala cakudya, sindidzamva kupfuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi cirala, ndi caola.

13. Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! taonani, aneneri ati kwa iwo, Simudzaona lupanga, simudzakhala ndi cirala; koma ndidzakupatsani mtendere weniweni mommuno.

14. Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, sindinauza iwo, sindinanena nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi cinthu cacabe, ndi cinyengo ca mtima wao.

15. Cifukwa cace atero Yehova za aneneri onenera m'dzina langa, ndipo sindinawatuma, koma ati, Lupanga ndi cirala sizidzakhala m'dziko muno; ndi lupanga ndi cirala aneneriwo adzathedwa.

16. Ndipo anthu amene adzanenera kwa inu adzaponyedwa kunja m'miseu ya Yerusalemu cifukwa ca cirala ndi lupanga; ndipo adzasowa akuwaika, ndi akazi ao, ndi ana ao amuna ndi akazi; ndipo ndidzatsanulira pa iwo zoipa zao.

17. Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukuru, ndi bala lopweteka kwambiri.

18. Ndikaturukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! ndikalowa m'mudzi, taonani odwala ndi njala pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.

19. Kodi mwakanadi Yuda? kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? bwanji mwatipanda ife, ndipo tiribe kucira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakucira, ndipo taonani mantha!

20. Tibvomereza, Yehova, cisalungamo cathu, ndi coipa ca makolo athu; pakuti takucimwirani Inu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 14