Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 13:3-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yaciwiri, kuti,

4. Tenga mpango umene unaugula, umene uli m'cuuno mwako, nuuke, nupite ku Firate, nuubise m'menemo m'phanga la m'mwala.

5. Ndipo ndinapita, ndinaubisa pa Firate, monga Yehova anandiuza ine.

6. Ndipo panali atapita masiku ambiri, kuti Yehova anati kwa ine, Uka, pita ku Firate, nukatenge kumeneko mpango uja, ndinakuuza iwe ukaubise kumeneko.

7. Ndipo ndinanka ku Firate, ndikumba, nditenga mpango m'malo m'mene ndinaubisamo; ndipo, taonani, mpango unaonongeka, wosayenera kanthu.

8. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,

9. Yehova atero, Momwemo ndidzaononga kudzitama kwa Yuda, ndi kudzitama kwakukuru kwa Yerusalemu.

10. Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu yina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.

11. Pakuti monga mpango uthina m'cuuno ca munthu, comweco ndinathinitsa kwa Ine nyumba yonse ya Israyeli ndi nyumba yonse ya Yuda, ati Yehova, kuti akhale kwa Ine anthu, ndi dzina, ndi cilemekezo, ndi ulemerero; koma anakana kumva.

12. Cifukwa cace uzinena ndi iwo mau awa: Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo; ndipo adzati kwa iwe, Kodi sitidziwitsa bwino kuti matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo?

13. Ndipo udzati kwa iwo, Atero Yehova, Taonani, ndidzadzaza ndi ciledzero onse okhala m'dziko muno, ngakhale mafumu onse amene akhala pa mpando wacifumu wa Davide, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi onse okhala m'Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 13