Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Rute 4:2-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo anatenga amuna khumi a akulu a mudzi, nati, Mukhale pansi apa. Nakhala pansi iwo.

3. Pamenepo anati kwa woombolerayo, Naomi anabwerayo ku dziko la Moabu ati agulitse kadziko kala kadali ka mbale wathu Elimeleki;

4. ndipo ndati ndikuululira ici, ndi kuti, Ugule aka pamaso pa nzika, ndi pamaso pa akulu a anthu a kwathu. Ukafuna kuombola ombola; koma ukapanda kuombola, undiuze, ndidziwe; pakuti palibe woombola koma iwe, ndi ine pambuyo pako. Pamenepo anati, Ndidzaombola.

5. Nati Boazi, Tsiku lomwelo ugula mundawo pa dzanja la Naomi, uugulanso kwa Rute, Mmoabu, mkazi wa wakufayo, kuukitsira dzina la wakufayo pa colowa cace.

6. Ndipo woombolerayo anati, Sindikhoza kuuombola kwa ine ndekha, ndingaononge colowa canga; udzitengere wekha mphamvu yanga yakuombola; popeza sinditha kuombola.

7. Koma kale m'Israyeli pakuombola ndi pakusinthana, kutsimikiza mlandu wonse, akatero: munthu abvula nsapato yace, naipereka kwa mnansi wace; ndiwo matsimikizidwe m'Israyeli.

8. Ndipo woombolayo anati kwa Boazi, Udzigulire wekha kadzikoko. Nabvula nsapato yace.

9. Nati Boazi kwa akulu, ndi kwa anthu onse, Inu ndinu mboni lero lino kuti ndagula zonse za Elimeleki, ndi zonse za Kilioni, ndi Maloni, pa dzanja la Naomi.

10. Ndiponso Rute Mmoabu, mkazi wa Maloni ndamgula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa colowa cace; kuti dzina la wakufayo lisaiwalike pakati pa abale ace, ndi pa cipata ca malo ace; inu ndinu mboni lero lino.

Werengani mutu wathunthu Rute 4