Ndipo Boazi anakwera kumka kucipata, nakhala pansi pomwepo; ndipo taona, woombolera winayo adanena Boazi analinkupita; nati iye, Iwe uje, pambuka, khala pansi apa; napambuka iye, nakhala pansi.