Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 22:3-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo Moabu anacita mantha akuru ndi anthuwo, popeza anacuruka; nada mtima Moabu cifukwa ca ana a Israyeli.

4. Ndipo Moabu anati kwa akuru a Midyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse ziri pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Moabu masiku amenewo.

5. Ndipo anatuma amithenga kwa Balamu mwana wa Beori, ku Petori, wokhala kumtsinje, wa dziko la anthu a mtundu wace, kuti amuitane, ndi kuti, Taonani, anaturuka anthu m'dziko la Aigupto; taonani, aphimba nkhope ya dziko, nakhala popenyana ndi ine.

6. Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawalaka, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapitikitse m'dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.

7. Ndipo akuru a Moabu ndi akuru a Midyani anamuka ndi mphotho za maula m'dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.

8. Ndipo ananena nao, Mugone kuno usiku uno, ndidzakubwezerani mau, monga Yehova adzanena ndi ine; pamenepo mafumu a Moabu anagona ndi Balamu.

9. Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu, nati, Anthu awa ali ndi iwe ndiwo ayani?

10. Ndipo Balamu anati kwa Mulungu, Balaki mwana wa Zipori mfumu ya Moabu, anatumiza kwa ine, ndi kuti,

11. Taonani, anthu awa adaturuka m'Aigupto aphimba nkhope ya dziko, idzatu unditembererere awa; kapena ndidzakhoza kulimbana nao nkhondo, ndi kuwapitikitsa.

12. Koma Mulungu anati kwa Balamu, Usapita nao; usatemberera anthuwa; pakuti adalitsika.

13. Ndipo Balamu anauka m'mawa, nati kwa akalonga a Balaki, Mukani ku dziko lanu; popeza Yehova andikaniza kuti ndisapite nanu,

14. Pamenepo akalonga a Moabu ananyamuka, nafika kwa Balaki, nati, Alikukana Balamu kudza nafe.

15. Koma Balaki anaonjeza kutumanso akalonga, ocuruka, ndi omveka koposa awa.

16. Ndipo anadza kwa Balamu, nati kwa iye, Atero Balaki mwana wa Zipori, Pasakhaletu cinthu cakukuletsa kudza kwa ine;

17. popeza ndidzakucitira ulemu waukuru, ndipo zonse unena ndi ine ndidzacita; cifukwa cace idzatu, unditembererere anthu awa.

18. Ndipo Balamu, anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Cinkana Balaki andipatsa nyumba yace yodzala ndi siliva ndi golidi, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kucepsako kapena kuonjezako.

19. Ndikupemphani, tsono, khalani pano inu usiku uno womwe; kuti ndidziwe comwe Yehova adzanenanso nane.

20. Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kumka nao, koma mau okha okha ndinena ndi iwe, ndiwo ukacite.

21. Pamenepo Balamu anauka m'mawa namanga buru wace, namuka nao akalonga a ku Moabu.

22. Koma anapsa mtima Mulungu cifukwa ca kupita iye, ndipo mthenga wa Yehova anadziika m'njira wotsutsana naye, Ndipo anali wokwera pa buru wace, ndi anyamata ace awiri anali naye,

Werengani mutu wathunthu Numeri 22