Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 18:18-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo nyama yace ndi yako, ndiyo nganga ya nsembe yoweyula ndi mwendo wathako wa kulamanja, ndizo zako.

19. Nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika, zimene ana a Israyeli azikweza kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna ndi kwa ana ako akazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; ndilo pangano lamcere losatha, pamaso pa Yehova, kwa iwe ndi mbeu zako pamodzi ndi iwe.

20. Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ulibe colowa m'dziko lao, ulibe gawo pakati pao; Ine ndine gawo lako ndi colowa cako pakati pa ana a Israyeli.

21. Ndipo taonani, ndawaninkha ana a Levi limodzi la magawo khumi mwa zonse m'Israyeli, likhale colowa cao, mphotho ya pa nchito yao alikuicita, nchito ya cihema cokomanako.

22. Ndipo kuyambira tsopano ana a Israyeli asayandikize cihema cokomanako, angamasenze ucimo kuti angafe.

23. Koma Alevi azicita nchito ya cihema cokomanako, iwo ndiwo azisenza mphulupulu yao; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; ndipo asakhale naco colowa pakati pa ana a Israyeli.

24. Popeza ndapatsa Alevi limodzi la magawo khumi, la ana a Israyeli, limene apereka nsembe, yokweza kwa Yehova, likhale colowa cao; cifukwa cace ndanena nao, Asadzakhale naco colowa mwa ana a Israyeli.

25. Ndipo Yehova ananena ndil Mose, nati,

26. Unenenso ndi Alevi, nuti nao, Pamene mulandira kwa ana a Israyeli, limodzi la magawo khumi limene ndakupatsani likhale colowa canu cocokera kwao, muziperekako nsembe yokweza ya Yehova, limodzi la magawo khumi la limodzi la magawo khumi.

27. Ndipo akuyesereninso nsembe yanu yokweza monga tirigu wa padwale, monga mopondera mphesa modzala.

28. Momweno inunso muzipereka kwa Yehova nsembe yokweza yocokera ku magawo anu onse a magawo khumi, a zonse muzilandira kwa ana a Israyeli; ndipo muperekeko nsembe yokweza ya Yehova kwa Aroni wansembe.

29. Mupereke nsembe zokweza zonse za Yehova kuzitenga ku mphatso zanu zonse, kusankhako zokometsetsa ndizo zopatulika zace.

Werengani mutu wathunthu Numeri 18