Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 6:6-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo adze nayo nsembe yace yoparamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda cirema ya m'khola mwace, monga umayesa mtengo wace, ikhale nsembe yoparamula, adze nayo kwa wansembe;

7. ndipo wansembeyo amcitire comtetezera pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa; kunena ziti zonse akazicita ndi kuparamula nazo.

8. Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,

9. Uza Aroni ndi ana ace, ndi kuti, Cilamulo ca nsembe yopsereza ndi ici: nsembe yopsereza izikhala pa nkhuni za pa guwa la nsembe usiku wonse kufikira m'mawa; ndipo mota wa pa guwa la nsembe uziyakabe pamenepo.

10. Ndipo wansembe abvale mwinjiro wace wabafuta, nabvale pathupi pace zobvala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, mota utanyeketsa nsembe yamoto pa guwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe.

11. Pamenepo abvule zobvala zace, nabvale zobvala zina, nacotse phulusa kumka nalo kunja kwa cigono, kumalo koyera.

12. Ndipo mota wa pa guwa la nsembe uyakebe pamenepo, wosazima; wansembe ayatsepo nkhuni m'mawa ndi m'mawa; nakonzepo nsembe yopsereza, natenthepo mafuta a nsembe zoyamika.

13. Moto uziyakabe pa guwa la nsembe, wosazima.

14. Ndipo cilamulo ca copereka caufa ndico: ana a Aroni azibwera naco pamaso pa Yehova ku guwa la nsembe.

15. Ndipo atengeko wodzala manja pa ufa wa copereka ca ufa wosalala, ndi pa mafuta ace, ndi libona lonse liri pa copereka caufa, nazitenthe pa guwa la nsembe, zicite pfungo lokoma, ndizo cikumbutso cace ca kwa Yehova.

16. Ndipo cotsalira cace adye Aroni ndi ana ace; acidye copanda cotupitsa m'malo opatulika; pa bwalo la cihema cokomanako acidye.

17. Asaciphike ndi cotupitsa, Ndacipereka cikhale gawo lao locokera pa nsembe zanga zamoto; ndico copatulikitsa, monga nsembe yaucimo, ndi monga nsembe yoparamula.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 6