Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 17:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, ucite cotetezera moyo wanu; pakuti wocita cotetezera ndiwo mwazi, cifukwa ca moyo wace.

12. Cifukwa cace ndinanena kwa ana a Israyeli, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu, kapena mlendo ali yense wakugoneramwa inu asamadya mwazi.

13. Ndipo munthu ali yense wa ana a Israyeli, kapena mlendo wakugonera pakati pa inu, akasaka nyama kapena mbalame yakudya, nakaigwira; azikhetsa mwazi wace naufotsere ndi dothi.

14. Pakuti ndiwo moyo wa: nyama zonse, mwazi wace ndiwo moyo wace; cifukwa cace ndinanena kwa ana a Israyeli, Musamadya mwazi wa nyama iri yonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndi mwazi wace; ali yense akaudya adzasadzidwa.

15. Ndipo ali yense wakudya yakufa yokha, kapena yojiwa kuthengo, ngakhale ndiye wa m'dziko kapena mlendo, azitsuka nsaru zace, nasambe ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo adzakhala woyera.

16. Koma akapanda kuzitsuka, kapena kusamba thupi lace, adzasenza mpholupulu yace.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 17